Anapulumuka ma bomba awiri

Uyu ndi Tsutomu Yamaguchi (1916-2010). Mu 1945 nthawi ya nkhondo yachiwiri yapa dziko lonse, ankakhala ku Japan ndipo anali Marine Engineer.

Pa 6 august, Tsutomu anapita kukagwira ntchito ku Hiroshima. Ali kumeneko, US inaponya bomba la atom, linapha anthu 140,000.

Tsutomu anavulala koma anapulumuka. Ananyamuka kumapita ku mzinda wina wa Nagasaki.

Atafika ku Nagasaki, US inaponyaso bomba lina pa 9 August ku Nagasaki ko. Linapha anthu 70,000.

Tsutomu Yamaguchi anapulumukanso. Boma la Japan linamupanga recognise ngati Hi-bakusha (opulumuka bomba lowopsyalo).

Anakhala moyo mpaka ukalamba, kumwalira mu 2010.

Next
Next

Mayi olusa wamangidwa